Zowonedwa ndi ambiri

Chithandizo kwa ife

Zolankhula za Imam Ali (a.s)7.


Zolankhula za Imam Ali (a.s)7.

( 0 Votes ) 

Zolankhula za Imam Ali (a.s)7.
Imam Ali adanena kuti:
إنّ لأهل الدِّین علاماتٌ یُعرفون بها:
صِدقُ الحدیث وأداءُ الأمانة و وفاءٌ بالعَهدِ و صِلةٌ للأرحام و رحمةٌ للضُّعَفاء وقِلّةُ مُؤاتاةٍ للنساء وبَذلُ المعروف وحُسنُ الخُلق و سَعَةُ الحِلمِ واتِّباعُ العلم وما یُقَرِّبُ مِن الله زُلفىَ فَطُوبىَ لهم وحُسنُ مَآبٍ.  
-Anthu omwe ali ndichipembedzo, kusonyeza kuti amamuwopa Mulungu ndikugwira ntchito yomwe akulamulira iye ndikusiya zomwe waletsa, ali ndi zizindikiro zomwe amadziwika nazo.
-Choyamba ndi kulankhula zoona. Kodi ndi anthu angati omwe aphedwa kapena kukumana ndi mavuto chifukwa cha bodza?
-Chachiwiri kubweza chinthu chamwini akamusungitsa.
-Chachitatu kukwaniritsa lonjezo.
-Chachinayi kulumikiza ubale.
-Chachisanu kumvera chisoni anthu omwe ali ofowoka. Munthu ngati ali mtsogoleri wa anthu ayenera kuyesetsa kuthandiza anthuwo munjira zosiyana siyana. Mulungu akunena kuti:
وَمَن قُدِرَ عَلَیْهِ رِزْقُهُ فَلْیُنفِقْ مِمَّا آتَاهُ اللَّهُ لَا یُکَلِّفُ اللَّهُ نَفْسًا إِلَّا مَا آتَاهَا سَیَجْعَلُ اللَّهُ بَعْدَ عُسْرٍ یُسْرًا  .
-Munthu yemwe zopeza zaumoyo wake zili zochepa komanso amazipeza movutikira, ayenera kupereka  molingana ndi zomwe Mulungu wamupatsa, Mulungu samulamula munthu kupanga ntchito yomwe sangayikwanitse  komanso samupempha munthu kupereka zomwe sadamupatse, dziwani kuti Mulungu adzawapanga mavuto kukhala ofewa.
-Chachisanu ndi chimodzi  kukwanitsa udindo wake pa banja lake komanso pakati pa  akazi omwe sali achibale ake( ghair mahram). Chifukwa kulankhulana kwa mwamuna ndi mkazi yemwe Sali m’bale wake popanda chifukwa chovomerezeka ndi zoipa (makruh). Kukhala limodzi ndi azimayi pagulu loletsedwa. Ngati mkazi angakhale pagulu lomwe pali amuna ndikupezeka kuti tsitsi lake likuwonekera kunja malo amenewo ndi oletsedwa kupezeka iye. Mkazi kuzikongoletsa ndikuziwonetsera kwa amuna ndizoletsedwa (haraam). Mkazi kaya avala zovala pofuna kuzikongoletsa kwa amuna ndizoletsedwa.
-Chachisanu ndi ziwiri kudzala zinthu zabwino pakati pa anthu.
-Chachisanu ndi zitatu makhalidwe abwino.
-Chachisanu ndi zinayi kupirira pamavuto mokwanira.
-Chakhumi kutsatira maphunziro ndi kuzindikira.
-Chakhumi ndi chimodzi  kutsatira zinthu zomwe zimamuyandikitsa munthu kwa Mulungu.
Mwayi ukhale kwa anthu omwe angakhale ndi zizindikiro zimenezi komanso iwowa ali ndi mapeto abwino.   

Kuwonjezera ganizogrey Zolankhula za Imam Ali (a.s)7.
zikhale zatsopano


sharethis Zolankhula za Imam Ali (a.s)7.

Kutumiza funso

ایمیل شما منتشر نمی شود.
Malo okakamizidwa kudzadzitsamo akudziwika ndi chizindikiro ichi * .

*


4 + = نُه

Kulumikizana ndi ife | RSS |Zolinga za Site

Ufulu onse wa Site yofalitsa uthenga ya Islam 14 ndi otetezedwa ndipo zikuloledwa kugwiritsa ntchito zinthuzi potchula komwe zachokera.