Zowonedwa ndi ambiri

Chithandizo kwa ife

Isil ithawa.


Isil ithawa.

( 0 Votes ) 

Isil ithawa.

grey Isil ithawa.
 
Wamkulu wa committee yachitetezo munzinda wa Diyal mdziko la Iraq wanena kuti kulimbana komwe kudabuka mderali pakati pa asilikali adzikoli komanso anthu wamba ozipereka ndi gulu la Isil komwe kudatenga maola okwana atatu kudapangitsa kuti gulu lina la Isil lithawe kuchoka mdera laSadiyyah povala zovala zachikazi.
Asilikali adziko la Iraq komanso anthu akufuna kwabwino adalimbana ndi gululi kwa maola atatu ndipo adakwanitsa kuchotsa gulu la Isil mderali lomwe lili pamtunda wa 60km kumpoto chakummawa kwa Baqubah.  
Asilikaliwa pamodzi ndi anthuwa adagwiritsa ntchito njira zosiyana siyana mpaka adakwanitsa kulowa malo omwe Isil imakhala ndikuwathira zipolopolo.
Iwowa pofuna kuthawa ndikuzemba zipolopolo zomwe zina zimachokera mundege za nkhondo amavala zovala zachikazi ndikumatuluka munzindawo.
Kenako adalengeza kuti nzinda wa Diyal watsukidwa ndi gulu la Isil.

Kuwonjezera ganizogrey Isil ithawa.
zikhale zatsopano


sharethis Isil ithawa.

Kutumiza funso

ایمیل شما منتشر نمی شود.
Malo okakamizidwa kudzadzitsamo akudziwika ndi chizindikiro ichi * .

*


× 3 = شش

Kulumikizana ndi ife | RSS |Zolinga za Site

Ufulu onse wa Site yofalitsa uthenga ya Islam 14 ndi otetezedwa ndipo zikuloledwa kugwiritsa ntchito zinthuzi potchula komwe zachokera.