Zowonedwa ndi ambiri

Chithandizo kwa ife

Chiwahhabi 7


Chiwahhabi 7

( 0 Votes ) 

Mudzina la Mulungu mwini chifundo ndi chisoni chosatha.
Mbiri za Muhammad bin Abdul Wahhabi
Muhammad bin Abdul Wahhabi ndi mapemphero, kusala, jihad ndi…
Chiwahabi ndi udani wawo ndi Chisilamu
Ndondomeko ya Chiwahabi pofuna kufafaniza Chisilamu.
Muhammad bin Abdul Wahhabi ndimunthu yemwe adafuna kuti dzina lake litchuke. Ndimunthu oti samalemekeza mashaikh ayi.
Henfry akunena kuti: Nthawi yomwe maina amashaikh adali kutchulidwa monga Abu Hanifa mashaikh ena adali kupereka ulemu kwa iye koma Muhammad bin Abdul Wahhabi samatero ayi, iye adali kunyoza angakhale maswahaba omwe. Iye amanena kuti mabuku amahadith monga Bukhari ndi opanda pake. Zikhulupiriro ngati zimenezi ndizomwe tikuona lero lino kuti dziko la America  kukupezeka mizikiti yomwe mashaikh ake omwe amatsogolera ndioti amalamulira ndikupanga zosalongosoka monga ukwati wa amuna okhaokha ndi zina ponena kuti mu Quran nkhani imeneyi sidanenedwe.
Henfry akupitiliza kunena kuti: Ine ndidakumana ndi Muhammad bin Abdul Wahhabi ndipo ndidali kukambirane naye za nkhani yachipembedzo, ndidamufunsa za jihad ndidati: Jihad siyokakamizika, adati chifukwa chiyani Mulungu akunena mu Quran kuti:
﴿یا أَیُّهَا النَّبِیُّ جاهِدِ الْکُفَّارَ وَ الْمُنافِقِینَ وَ اغْلُظْ عَلَیْهِمْ وَ مَأْواهُمْ جَهَنَّمُ وَ بِئْسَ الْمَصِیر﴾ (التوبة:۷۳)
E iwe Mtumiki! Limbana ndi anthu okanira za Mulungu komanso amthira kuwiri ndipo uwalimbire mtima posawamvera chisoni,malo awo iwowa ndikumoto wa Jahannama, ndiye malo  awo obwelerawa oipa bwanji.
Ndidati ngati zilichoncho chifukwa chiyani Mulungu sadachite jihad ndi amthira kuwiri? Adati: Mtumiki amachita jihad ndi iwo  kudzera mmawu, ndidati: Ndiye kuti jihad ndi anthu okanira iyenera kukhalanso yapakamwa, nanga ndichifukwa chiyani Mtumiki adamenya nawo nkhondo, adati: Mtumiki adamenya nawo nkhondo pofuna kuziteteza kuchokera ku ziwembu zawo.
- Kenako ndidamfunsa kuti Muti’a (ukwati wanthawi yayifupi) ndiyololedwa, adati ayi, ndidati: nanga ndifukwa chiyani Mulungu mu Qurani akunena kuti:
﴿فَمَا اسْتَمْتَعْتُمْ بِهِ مِنْهُنَّ فَآتُوهُنَّ أُجُورَهُن﴾ (النساء:۲۴)
Akazi omwe mukhale nawo ndikuthandizika nawo apatseni malipiro awo
Adati Khalifa wachiwiri adaletsa Muti’a, adati:
))متعتان کانتا علی عهد رسول اللَّه و أنا احرّمهما و اعاقب علیهما: متعة النساء، و متعة الحجّ((.  کافی (ط – دار الحدیث) / ج‏۸ / ۱۶۳ / ۲۷ – باب حج النبی صلى الله علیه و آله ….. ص : ۱۵۸٫
Nthawi ya Mtumiki (s.a.w.w) kudali mamutia awiri koma ine ndikwapanga kukhala oletsedwa ndipo ndidzamulanga yense opanga iwo, mutia ya akazi ndi yahajj.
Ndidamufunsa kodi zikutheka bwanji kuti iwe ukumvera maganizo akhalifa wachiwiri ndikusiya Quran ndi Mtumiki chifukwa zinthu ziwirizi zikuloleza Mutia pomwe Khalifa wachiwiri adaletsa, kodi zinthu ziwirizi ndizapamwamba kapena khalifa wachiwiri? Adakanika kuyankha ndipo adakhala chete.  Kenako ndidatengerapo mwayi pomuona kuti adali wachinyamata komanso adalibe mkazi ndidati kwa iye, bwanji ndikupezele mkazi kuti ukale naye mwakanthawi? Adayang’ana pansi kenako ine ndidamufuna mkaziyo, Mkaziyu adalowa mnyumba yake Muhammad bin Abdul Wahhabi ndipo dzina lake adali Swafiyya (mmodzi mwa akazitape( ndipo adakhala naye akuchita ukwati wanthawi yayifupi.
Zikutheka bwanji munthu yemwe sakhulupirira za mutia akukachita mutia???
Inde ndizikhulupiriro ngati zimenezi ndizomwe zidapangitsa kuti munzinda wa Alexandria gulu la asilamu ligonje chifukwa cha mowa ndi akazi.
- Tsiku lina ndidamufunsa za mowa ndidati kodi ndizoona kuti mmodzi mwa maswahaba amtumiki amamwa mowa? Kodi onsewa adali osokonekera koma iwe ndiolondola? Adakanika kuyankha.
- Kodi ndizotheka kuti mowa omwewu ukhale ololedwa muchipembedzo china pomwe muchipembedzo china ukhale oletsedwa? Kumachita kuti zonsezi ndizipembedzo zochokera kwa Mulungu? Inu mmodzi mwa akulu akulu anu amamwa mowa ndipo amanena kuti kumwa mowa ndikusaledzera palibe vuto, Muhammad adasowa choyankha kenako Swafiyya adabweretsa mowa wambiri ndikumpatsa Muhammad bin Abdul Wahhabi ndipo iye adamwa.
Kenako ndidanena kuti kusala mmwezi wa Ramadhan sikokakamizika, adati chifukwa chiyani? Ndidati :chifukwa Mulungu akunena kuti:
﴿و أَنْ تَصُومُوا خَیْرٌ لَکُمْ إِنْ کُنْتُمْ تَعْلَمُون﴾ (البقرة:۱۸۴)
Mukasala ndizabwino kwa inu mudakadziwa
Sadanene mu ayayi kuti kusala ndikokakamizidwa. Komabe iye adalimbalimba pamenepa.
Kenako ndidamufunsa za mapemphero kuti mapemphero ndiosakakamizika, adati chifukwa chiyani, ndidati: chifukwa choti Mulungu akunena kuti:
﴿وَ أَقِمِ الصَّلاةَ لِذِکْرِی﴾ (طه:۱۴)
Imikani mapemphero ndicholinga choti mundikumbukire.
Mwachoncho mutha kumukumbukira Mulungu popanda kupemphera.
Kuchokera apa Muhammad bin Abdul Wahhabi mapemphero ake adayamba kufooka.
- Kenako ine ndidamufotokozera iye za maloto omwe ndidalota: Ndidalota Mtumiki atakhala padzuwa ndipo mashaikh adakhala mmbali mwake omwe sindimadziwa, kenako iwe udalowa nkhope yako ikunyezimira ndipo Mtumiki adadzuka ndikukupatsa ulemu ndikukupsopsona pamphumi pako ndikukuwuza kuti: iwe ndi otsatira wa ine komanso mlowammalo wakuzindikira kwanga ndipo udzakhala mlowammalo wanga, iwe udati: e  Mtumiki! Ndikuopa kuti ndidzaonetsere kwa anthu kuzindikira komwe ndili nako, Mtumiki adakuwuza kuti: Usaope chifukwa ndiwe wapamwamba kuposa iwo.
Nditamaliza kunena zimenezi adakondwa kwambiri moti adali kujowa akunena kuti: ndizoona? Ndizoona?
Kuyambira tsiku limeneli adatsimikiza  zofalitsa zikhulupiriro zake pakati pa anthu.

Kuwonjezera ganizogrey Chiwahhabi 7
zikhale zatsopano


sharethis Chiwahhabi 7

Kutumiza funso

ایمیل شما منتشر نمی شود.
Malo okakamizidwa kudzadzitsamo akudziwika ndi chizindikiro ichi * .

*


7 − = شش

Kulumikizana ndi ife | RSS |Zolinga za Site

Ufulu onse wa Site yofalitsa uthenga ya Islam 14 ndi otetezedwa ndipo zikuloledwa kugwiritsa ntchito zinthuzi potchula komwe zachokera.