Zowonedwa ndi ambiri

Chithandizo kwa ife

Chiwahhabi 8


Chiwahhabi 8

( 0 Votes ) 

Mudzina la Mulungu mwini chifundo ndi chisoni chakuya.
Kukumana kwa kasanu ndi zitatu pa mutu wa Wahabiyyat
Maganizo a kulu akulu achi Shia pa mutu wa Wahabiyyat ndi Al Su’di
Maganizo a kulu akulu a Ahlusunnat pa mutu wa Wabiyyat ndi Al Su’di
Wahabiyyat mukuyang’ana kwa Imam Khumaini, Khamenei, Ayatu Idham, Fadhil Lankarani, Makarim Shirazi ndi ena…
Wahabiyyat ndi likulu la zoipa, ukazitape, Kubadwa kwa Chiyuda, kupha, kuononga Chisilamu, kumenya nkhondo ndi Chisilamu, kumanga ubale ndi Ayuda, kusiyanitsa Asilamu, kuwagwiritsa ntchito moipa  Asilamu, kufuna kuononga Ka’aba
Ibn Tayimiyya: Vuto lanzeru ndikuganiza, okazikitsa bidiat (kubweretsa zinthu zomwe muchipembedzo mulibe)
Ahlubait: Kunyoza malo olemekezeka a Chisilamu, Kunja kwa Chisilamu

1- Imam Khumaini adalankhula pamwambo omwe adali kukumbukira anthu omwe adaphedwa  lachisanu mchaka cha 1366 omwe eni ake adawatcha “Shuhadaye Jumue Khunin” kuti: Kodi asilamu adziko lapansi angayiwale zakuphedwa kwa anthu ophunzira aChisilamu ambiri, akazi ndi mahujjaj( anthu omwe adapita kukapanga hajji) ndi Al Su’di omwe amazitcha kuti ndi Khadimul Haramain. Kodi Asilamu sakuona kuti malo onse omwe ma Wahhabi alinawo  asanduka malo ochitira ukazitape ndintchito zoipa, inu simukuona kuti Al Su’di akupanga ubale ndi Israel ndikwauza kuti tipanga udani ndi Iran. Inu simudamve kulankhula kwa anthu ofuna kufafaniza Chisilamu kuti kulibwino kusamala ndikuteteza Su’udi Arabia kusiyana ndi Israel chifukwa choti ngati Al Su’di atakwanitsa kusokoneza Asilamu dziko lonse ndiye kuti zolinga zathu zakwanilitsidwa.
Kodi zochitika ngati zimenezi sizikuchotsa ulemelero wa Chisilamu?
Kodi Asilamu akangokhala osachita kanthu sikulakwa ayi?
Kodi palibe Msilamu yemwe angadzuke kuchitapo kanthu?
Mkuluyu mu will yomwe adalemba adati: Ife tikuona kuti Mfumu Fahad chaka chilichonse akuononga ndalama zambiri pokhazikitsa malo ndikulalikira zofuna kuononga Chisilamu.
2- Khameneni mukulankhula kwake adati: Anthu ofuna kufafaniza Chisilamu adakhonza gulu limeneli la Chiwahabi ndipo akuligwiritsa ntchito pofuna kuononga umodzi wa Asilamu ndikukhazikitsa likulu lakupanga zoipa ku Israel. Iwo akuyesetsa kuti Chiwahabi chilowelere pakati pa Asilamu dziko lonse lapansi ndikuwasokoneza posiya Chisilamu chowonadi ndikuyamba kutsatira Chisilamu chabodza chawo. Inu simukuona kuti Al Su’di akugwirizana ndi ndale za America komanso apanga nawo ubale. Inu simudaone Malik Abdullah akumwa mowa limodzi ndi Bush?
3- Fadhil Lankarani: Mukulankhula kwake mchaka cha 1386 adati: Ma Wahabi ndi kochokera kwa kufr, kuononga Chislamu, adakhonzedwa pofuna kubweretsa kusiyana maganizo pakati pa Asilamu, iwowa cholinga chawo ndikuononga Ka’aba, manda aMtumiki Quran ndi Chisilamu, Mashaikh onse amipatuko yosiyanasiyana  ndiogwirizana pazakuti Chiwahhabi chili kunja kwa Chisilamu.
4- Makarim Shirazi: Adani aChisilamu adakhonza Chiwahhabi ndicholinga chofuna kubweretsa kusiyana maganizo pakati pa Asilamu, kugwiritsa ntchito moipa Asilamu, Chiwahhabi ndilimodzi mwa mavuto omwe Chisilamu chakumana nalo munthawi yayitali.
5- Swafi Ghulpaigani: Mawahhabi ali ndiudani ndi Mtumiki komanso Ahl Bait, iwowa adabwera pofuna kuononga Chisilamu, koma chomwe ayenera kudziwa ndichoti Chiwahhabi chimenechi chitha posachedwapa ndipo zomwe zingatsala ndizoipa zawo zomwe akhala akuchita mmadera osiyanasiyana.
AKULU AKULU ASUNNI
1- Ibn Batuta:Mu bukhu lake la Rihlatu Ibn Batuta vol.1 page 57akuti: Munzinda wa Damashiq ndidamuona mmodzi mwa mashaikh a mathihab a Hanbal otchedwa Ibn Taimiyya ndipo adalikulankhula zambiri zachisilamu koma ndidazindikira kuti munthu ameneyu nzeru zake sizimayenda bwino.
2- Muhammad Bukhari Hanafi yemwe adabadwa mchaka cha 841A.H adati: Munthu wina aliyense yemwe angakhale ndichikhulupiriro choti Ibn Tayimiyya ndi Shaikhul Islam ndi okanira za Mulungu.
3- Ibn Hajar Makki yemwe adamwalira mchaka cha 874 A.H mu bukhu lotchedwa Al Fatwal Hadithiyyah  page 86 adati: Mulungu adampanga Ibn Tayimiyya kukhala wakhungu, osamva ndi osochera  ndipo mashaikh onse amathihabu anayi Sha’afi, Hanbal, Hanafi ndi Maliki amatsimikiza  zakuyipa kwa maganizo ndizikhulupiriro zake. Zolankhula zake ndizopanda pake komanso zosochera,iye adabweretsa Bidiat yambiri muchisilamu. Mulungu atichinjirize kuzikhulupiriro zake komanso amuweruze moyenera.
4- Ibn Hajar Askalani adati: Munthu wina aliyense yemwe angakhulupirire za zikhulupiriro za Ibn Tayimiyya moyo ndiololedwa kuphedwa.
5- Hasni Damashiqi: Mubukhu lake la Aswiratul Mustaqim Akuti: Ibn Tayimiyya yemwe ena amamutcha Nyanja ya maphunziro ndi oti ena mwa omutsatira ake amamutcha munthu wakunja kwachipembedzo. Chifukwa choti iwo pambuyo pochita kafukufuku mozama paza zikhulupiriro zake iye adampeza kuti amawachita Takfir popanda maumboni ogwira mtima asilamu ena komanso ndikusocheretsa ena.
Ibn  Tayimiyya amati: munthu amene angapemphe chithandizo kuchokera kwa munthu yemwe adamwalira ndikafir.Kodi ife kupempha kwa Mulungu kudzera kwa Mtumiki wathu ndiukafiri? Kodi Mtumiki zolankhula zathu samamva? Nanga pamapemphero athu atsiku ndi tsiku tikamati (assalamu alaika ayyuha nnabiyy warahamatullah wabarakatuh) zili bwanji?
6- Zubki  yemwe adamwalira mchaka cha 756 A.H mubukhu la Twabaqatu Shafi’iyyah vol. 9 page 253 akuti: Iye adabweretsa bidiat yomwe yatsekereza kugwiritsa ntchito kwa Asilamu sunnat ya Mtumiki (s.a.w.w), nsichi za Chisilamu adaononga, zokamba zake zikutsutsana ndi mashaikh onse muchisilamu, ndipo iyeyu angakhale mmagulu okwana 73 aja ali kunja.
7- Thahabi akuti:
Iye mu kalata yomwe adamulembera  Ibn Tayimiyya adati: Iwe munthu osauka, onse amene amakutsatira iwe ndi anthu opanda nzeru komanso operewera, otsatira IbnTayimiyyah ndi anthu ochita ziwembu. Ngati iwe ukutere ndi ine amene ndili nzako nanga adani ako udzawatani? Ndithudi adani achisilamu ndi ambiri mwachoncho pakati pako ndikuona anthu omwe ndi abodza, ndiochita zoipa okha okha.

Kuwonjezera ganizogrey Chiwahhabi 8
zikhale zatsopano


sharethis Chiwahhabi 8

Kutumiza funso

ایمیل شما منتشر نمی شود.
Malo okakamizidwa kudzadzitsamo akudziwika ndi chizindikiro ichi * .

*


9 − چهار =

Kulumikizana ndi ife | RSS |Zolinga za Site

Ufulu onse wa Site yofalitsa uthenga ya Islam 14 ndi otetezedwa ndipo zikuloledwa kugwiritsa ntchito zinthuzi potchula komwe zachokera.